Namadingo – Pefekiti Lyrics
Namadingo
[Verse 1]
Ndiloleni ndinene zoona zamkaziyu
Chili chonse chili muchimake pefekiti
Mlingo oyezedwa bwino
Thupi logwilana bwino
Pachingelezi
Kompakiti
Ndipo sindi kusamala
Za mkazi wina kupatula uyu
Ena ndikuwathila doom
Ma insekiti
Kandalama komwe ndinapeze
Pakutha pa mwezi
Tizankala pansi together
Kumenya ma bajeti
Tikalipila ya nyumba ya rent
Kwina ku tikumanga yathu
Kukabwela change shopping
Ku super maketi
Ona zako ndizanga baby
Palibe ichi ndichaine ndekha
Chili chonse ndi chako
Olo yanga waleti
Baby uli pefekiti
[Chorus]
Yemwe amati kulibe pefekiti
Akazakuona khope yako baby
Yemwe amati sadaone pefekiti
Akazakuona thupi lako baby
Azatula pasi udindo wabungwela
Impefekiti
Kuli kuvomereza kuti kuli ma pefekiti
Azatula pasi udindo wabungwe
Lopezerana zifukwa
Kuvomereza kuti kuli ma pefekiti
Yemwe amati kulibe pefekiti
Akazakuona khope yako baby
Yemwe amati kulibe wapefekiti
Akazakuona thupi lako baby
Azatula pasi udindo wabungwela
Impefekiti
Kuli kuvomereza kuti kuli ma pefekiti
Kuli pefekiti
Pefekiti
Kuvomereza kuti kuli ma pefekiti
Pefekiti
[Verse 2]
514898 iyi yanga pasiwedi
Gwira gwira phone baby
Palibe zopangana cheat
I love you for real
Now and forever more
Osandikaikira sindine sasipekiti
Ona zakale zapita zasala
Zasopano za awiri baby
No ma drama
No chipwilikiti
Ndipo singalole wina
Akujaile akuseweresa my first lady
Ulemu wako
Risipekiti
Mawa tipite ku mpingo
Kaya ku khoti tikasaine marriage certificate
Chimodzi modzi katundu ugula mu shop
Umboni ndi ma lisiti
Sizongotengana panjira
Opanda protocol (protocol)
Ngati malonda ogula kwamavenda
Muma street
Timasuke tipange mwana
Azinditchula adadi
Umaziwa ka marriage prodakiti
Pang’ono ndi pang’ono baby
Sikulina tizakweza range
Koma lelo tiza kwera ka sitaleti
Uli pefekiti
[Chorus]
Yemwe amati kulibeko pefekiti
Akazakuona khope yako baby
Yemwe amati sadaone wapefekiti
Akazakuona thupi lako baby
Azatula pasi udindo wabungwela
Impefekiti
Kuli kuvomereza kuti kuli ma pefekiti
Azatula pasi u chairman wabungwe
Lopezerana zifukwa
Kuvomereza kuti kuli ma pefekiti
Uli pefekiti
Uli pefekiti
Iwe gelo mmm hmm
(Iwe gelo mmm hmm)
Ona tumaso twako
(Tumaso twako)
Tioneka (tioneka)
Ngati nyenyezi gelo
Yamamawa gelo
Timawu twako (timawu twako)
Tumaveka ngati angeli baby
Akumwamba baby
Koma yemwe amati sadaone pefekiti
Azaone khope yako lako baby
Yemwe amati kulibe pefekiti
Like what you see? Support Ulwimbo by sharing this post and following us on Facebook, Instagram, Twitter, or Blogovin.
Track Info
Title | Pefekiti |
Artist | Namadingo |
Released | December 25, 2020 |
Producers | Moshu |
Genre | Afro Pop/Soul |